Ndiye ndi mawu amene akupezeka pa Genesis 1:1 china chilichonse m’moyo chikupatsidwa maonekedwe ake, cholinga chake komanso tanthauzo lake. Ndi chinthu chofunikila komanso kudzichepetsa kuzindikila kuti nkhani ya Baibulo siyidayambe ndi ife. Imayamba ndi Mulungu. Ndi chinthu chofunikila kwambiri kuzindikila kuti pamene nkhani ya masamba a Baibulo ikutambasulidwa ndi nkhani ya Mulungu. Iye wayima pakatipati pa zochitika zonse. Iye ali ndi magawo ofunikila. China chilichonse chikudalira Iye. Nkhaniyo ikuyenda monga mwa chifunilo chake komanso dongosolo lake. Zonse ndi za Iye, zochokela kwa Iye, kudzera mwa Iye, komanso zokhudzana ndi Iye.
Ndiye pamenepa titha kupezapo yankho pa funso lathu: ndi chifukwa chiyani Baibulo lidalembedwa? Ndiye mwachidule, Baibulo lidalembedwa kuti lionetsele ulemelero wa Mulungu.
Pa Habakuku 2:14 timawelenga kuti “Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziwitso cha ulemelero wa Yehova, monga momwe madzi amadzazira nyanja.”
Cholinga chachikulu cha Mulungu polenga komanso kuombola dziko ndi ulemelero wake. Nkhani ya Mulungu cholinga chake ndi kubweletsa ulemelero kwa Mulungu. Tikakumbukila kuti ulemelero wa Mulungu ndiye cholinga cha nkhani ya chiombolo, titha kulingalira zoyenela pa moyo wathu, pa ntchito yathu, pa kudzipeleka kwathu, komanso pa zimene tikwanilitsa.