Listen

Description

Khristu ndiye mutu wa mpingo. Akolose 1:18 akunena kuti: Iye ndiyenso mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi chake, woyamba kuuka kwa akufa, kuti Iyeyo akhale wopambana zonse.

Nanga izi zikutanthauzanji pa zochitika za pa mpingo? Zikutanthauza kuti mpingo ukuyenela kumvera Mawu a Khristu pa china chilichonse chimene mpingo umachita. Pamapeto pa zonse, Khristu ndiye amene “amayendetsa” mpingo osati abusa anu kapena akuluampingo anu. Abusa ndi akuluampingo akuyenela kutsogolera mpingo momvera Mawu ake a Khristu basi. Mpingo ukuyenela kutsatila cholinga cha Khristu, osati zina.

Ndiye funso lina nkumati, ngati Khristu ndi mutu wa mpingo, ndi chifukwa chiyani tili ndi anthu amene amasankhidwa ngati azitsogoleri m’mipingo mwathumu?

Kuyankha kwake tinene kuti: tili ndi azitsogoleri chifukwa choti Mulungu adatipatsa chitsanzo m’Malemba Opatulika za m’mene mipingo ikuyenela kuyendetsedwela. Makamaka, Mulungu akutiuza m’Mawu ake kuti tikhale ndi akulu komanso ma deacon osankhidwa m’mipingo mwathumu.