Tiyeni tiwerenge Mateyu 22:34-40
“Koma pamene Afarisi adamva kuti Iye adasowetsa chokamba Asaduki, adasokhana pamodzi. Ndipo m’modzi wa iwo, mphunzitsi wa chilamulo, adamfunsa Iye funso kuti amuyese Iye. ‘Mphunzitsi, lamulo lalikulu ndi liti la m’chilamulo?’ Ndipo Iye adati kwa iye, ‘Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse ndi maganizo ako onse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiwiri lofanana nalo ndi ili, Uzikonda mzako monga iwe mwini. Pa malamulo awiriwa pamatsamila chilamulo chonse ndi aneneri.’”
Pa ndime imeneyi, Yesu akunena kuti chilamulo chonse komanso zolemba zonse za aneneri zifupikitsidwa mu malamulo awiri amenewa – kukonda Mulungu komanso kukonda anthu ena. Mu njira ina titha kunena kuti chipangano chakale chonse chifupikitsidwa m’ma vesi amenewa.
Fundo yofunika kuyigwilitsitsa ndi yakuti: ngakhale chipangano chakale ndi chotalika komanso chovuta kusakatula ndi mabuku ambiri, Yesu adakwanitsa kulifupikitsa m’malamulo awiri amenewa.
Ndime ina imene titha kuyiona ndi Yohane 5:39-40
“Mumasanthula m’malembo, popeza muganiza kuti mwa iwo muli nawo moyo wosatha; ndipo iwo omwewo akundichitira Ine umboni, koma simufuna kubwera kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.”