Listen

Description

Tiyambe kuona za chipulumutso. 2 Timoteo 3:12-15. “Zoonadi, onse akufuna kukhala moyo wachiyero mwa Khristu Yesu, adzazuzidwa pamene anthu woyipa ndi wonyenga, adzayipa chiyipile, kunama ndi kunamizidwa. Koma iwe, ukhalebe mu zinthu zimene waziphunzira, ndi kuzikhulupilira motsimikizika, podziwa amene adakuphunzitsa ndi m’mene kuyambira umwana wako wadziwa malembo wopatulika, wokhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, kudzera mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.”

Chinthu chimodzi chofunikila kwambiri chimene tikuyenela kudziwa ndi chakuti Malemba Opatulika ali ndi kuthekela “kukupatsa nzeru kufikila chipulumutso kudzera m’chikhulupiliro cha mwa Yesu Khristu."