Listen

Description

Ndime imene tiyambe kuwerenga ndi Yakobo 2:14-26. “Chipindulo chake n’chiyani, abale anga, munthu akanena kuti ali nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupiriro chotere chikhoza kumpulumutsa? Ngati mchimwene kapena mlongo wavala movetsa chisoni, nasowekela chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu nanena nawo, ‘Mukani ndi mtendere, mukafunditsidwe ndi kukhuta,’ osawapatsa iwo zosowa za ku thupi; kupindula kwake n’chiyani? Momwemonso chikhulupiliro pachokha, chikapanda kukhala nazo ntchito, chili chakufa.

Koma wina atha kunena, ‘Iwe uli nacho chikhulupiliro, ndipo ine ndiri nazo ntchito.” Tandionetsa ine chikhulupiliro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuwonetsa iwe chikhulupiliro changa kudzera m’nchito zanga. Ukhulupilira iwe kuti Mulungu ali m’modzi; uchita bwino. Ngakhala ziwanda zikhulupiliranso— ndipo zinthunthumira! Kodi ufuna kuonetsedwa, munthu wopusa iwe, kuti chikhulupiliro chopanda ntchito chiri chakufa? Kodi Abrahamu kholo lathu, sadayesedwa wolungama ndi ntchito kodi, pamene adapereka mwana wake Isake pa guwa? Utha kuona kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo chikhulupiriro chidatsimikizika ndi ntchito zake; ndipo Malemba Opatulika adakwanilitsidwa wonena kuti, ‘Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye ngati chiyero’—ndipo adatchedwa bwenzi la Mulungu. Utha kuona kuti munthu ayesedwa wolungama mwa ntchito, osati ndi chikhulupiriro chokha. Ndipo momwemonso kodi Rahabi mkazi wadamayo sadayesedwa wolungama ndi ntchito pamene adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira yina? Pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.”

Buku la Yakobo ndi buku losangalatsa pa zifukwa zambiri; chifukwa chimodzi mwa izo ndi kuvetsetseka kwake. Limakamba zinthu mosaphiphilitsa. Kwa amene tikuyamba kumene kuwerenga Baibulo mokhazikika, buku limeneli ndi poyambila pabwino. Tidzakamba zambiri pa nkhani imeneyi m’ma program akutsogoloku.

Chimene tikufuna tione ndi chakuti Yakobo akukamba moveka bwino pa za chikhulupiliro komanso ntchito. Chimene akukamba ndi chakuti, “Ngati mumakhulupilira mwa Yesu, mumabala ntchito zolungama.

Koma pamenepa Yakobo sakunena kuti ntchito zanu zimakupangani kukhala olungama kapena kuti ntchito zanu zimakupulumutsani, ayi. Pamenepa ndi pofunika tivetsetse ndithu choonadi chimenechi. Inde Yakobo akukamba kunena kuti chikhulupiliro chenicheni chimabweletsa ntchito, koma sakunena kuti ntchito zathu nthawi zonse zimachokela pa chikhulupiliro chenicheni.

Kutanthauza kunena kuti, anthu ena atha kuchita ntchito zabwino zambiri, koma atha kuchita ntchito zabwinozo ndi zolinga zodzikonda okha. Tikayembekeza kuti ntchito zathu zabwino zitipanga kukhala olungama pamaso pa Mulungu tikusemphana nazo.