Lero tiyeni tiyambe ndi kuona mitundu ya Chipangano Chatsopano. Ndidatchula magawo anayi akuluakulu: Uthenga Wabwino, Mbiri, Makalata, komanso Mavumbulutso a Chimalizilo.
Magawo amenewa titha kuwatambasula motere:
Ø Uthenga Wabwino ndi mabuku anayi oyambilira a m’Chipangano Chakale. Mateyu, Marko, Luka komanso Yohane. Mabuku amenewa amatifotokozera zimene adaona za moyo, imfa, komanso kuuka kwa Yesu Khristu. Ndipo iwo akulemba izi monga nkhani.
Ø Tikafika ku Mbiri: Buku la Machitidwe limafotokozela chiyambi cha mpingo wakale, kutsatira imfa ya Khristu. Luka ndiye amene adalemba buku la Machitidwe. Ndipo buku limeneli limatengedwa kuti ndi lotsatila Uthenga Wabwino wa Luka.
Ø Tikafika ku Makalata: Makalata amenewa amakamba za tanthauzo la ntchito ya Yesu imene adayimaliza ya chikhulupiliro chathu komanso moyo wa tsiku ndi tsiku. Kalata ina iliyonse imathandizila owerenga kalatayo kumvetsetsa chiphuzitso cholondola komanso kuchenjeza mipingo pa za chiphuzitso chabodza.
Ø Tikakamba za Mavumbulutso a Chimalizilo: Buku la Chibvumbulutso lili m’gulu limeneli. Zithuzi zimene zikupelekedwa komanso zolembedwa mu buku limeneli ndi zovuta ndithu kuvetsa, koma tidziwe kuti bukuli limatiphuzitsa choonadi chakuti Yesu Khristu adzabwelanso kudzagonjetsa Satana kwamuyaya ndi kutenga ana ake kwawo.
Tifike pa gawo lina lotithandizila kuwerenga Baibulo ndilo: kufotokozela ndime za m’Baibulo kuti zivetsetseke bwino.
Ø Tikamakamba za kufotokozela tikunena za m’mene tingatanthauzile ndime zosiyanasiyana za Malemba Opatulika.
Ø Sabata yatha timaona zochitika m’ndime komanso kuzindikila za kufunika kwa zimene zikuchitika pamene tikuwerenga Baibulo. Ndiye titha kuona kuti pali kulumikizana pa nkhani ya kufotokozela komanso zochitika m’ndime imene tikuwelenga ya Baibulo.
Funso litha kufunsidwa kunena kuti, kodi zinthu ziwiri zimenezi zikulumikizana motani?
Ø Tikakamba za kufotokozela ndiye kuti tikufuna tione zimene zidachitika pamene nkhaniyo inkachitika ndi cholinga choti tithe kutanthauzila Baibulo moyenelera. Timaona nkhani ya amene adalemba, nthawi imene Malemba Opatulika adapelekedwa, komanso anthu oyamba amene adalandila mawuwo ndipo zonsezi cholinga chake ndi chakuti tithe kufotokozela komanso kutanthauzila moyenelera.
Ø Mu njira ina titha kunena kuti, sabata yatha pa zitsanzo zimene tidaona timayeselera m’mene tingafotokozele ndime ya m’Baibulo koma mwina sitidazindikile. Timatanthauzila Malemba Opatulika motsatila zochitika pa ndimeyo. Kutero ndiye kuti tikufotokozela.
Gawo lina limene lingatithandizile kuwerenga Baibulo ndiye kufunsa mafunso.
Njira imodzi yosavuta pamene tikuyamba kutanthauzila Malemba Opatulika ndiye kufunsa mafunso. Pali mafunso ambiri amene tingafunse pa ndime ina iliyonse komanso njira zina zimene titha kugwiritsa ntchito, koma mafunso atatu oyambila amene tingafunse pa ndime ina iliyonse ndi awa:
Ø Kodi ndimeyi ikundiuza zotani zokhudzana ndi Mulungu?
Ø Kodi ndimeyi ikundiuza zotani zokhudzana ndi anthu ena?
Ø Kodi ndimeyi ikundiuza zotani zokhudzana ndi ine?
Ø Ndiye tiyeni tiyesele kufusa mafunso amenewa pa ndime imodzi.