Listen

Description

LERO TIKUFUNA TIONE KUTI KODI TIPEMBEDZE MOTANI NDI MPINGO WATHU?

Tikudziwa chifukwa chimene mpingo ukuyenelera kukumana pamodzi. Koma ndi zinthu ziti zimene zingapangitse anthu kulephela kukumana ndi anzawo nthawi ya chipembedzo?

Pali zifukwa zingapo zimene zingapelekedwe zolepheletsa anthu kukumana ndi anzawo nthawi ya chipembedzo. Ena amanena kuti iwo amaonetsela chikhulupiliro chawo mu njira zina. Ena amanena kuti sadapeze mpingo owasangalatsa. Ena amanena kuti sasangalatsidwa ndi ulaliki wa abusa awo. Ena amanena kuti samva kulandilidwa ku mpingo kwawo. Ena mukawafusa nthawi zonse amangoti ndi nadwala ndiye nkumadabwa kuti kodi abale muzingodwala pasabata pokhapokha?

Ena amanena kuti alibe nthawi yopita ku tchalitchi. Ali ndi nthawi yochita china chilichonse koma ikafika nthawi yak u tchalitchi akuti alibe nthawi. Ndiye nkumati, Mulungu adakupatsani masiku 6 oti mutha kugwila ntchito zanu zonse. Ndipo adalamulira kuti mupatule tsiku limodzi lokha kumupembedza iye. Tsono mukufuna tsiku la Mulungulo mugwilenso ntchito zanu, zoona?

Ngati anthu okhulupilira, tikuyenela kuti tisakhale opanda chidziwitso komanso tisanyozele malamulo a Mulungu pa nkhani yokumana pamodzi ngati mpingo nkumapeza zifukwa zosaveka bwino kuti tisapite ku tchalitchi.

Tiyeni tione zinthu zina zimene anthu amawiringula kapena sazikonda zokhudzana ndi nthawi ya chipembedzo.

Ndinakamba kale kuti mwina anthu sangakondwele ndi ulaliki. Mwina amaona ma ulaliki kukhala otopetsa. Ena mwina kayimbidwe ka nyimbo, nyimbo zimene zimasankhidwa, machitidwe ena kapena kayankhulidwe kena kooneka kachikalekale mwina, mwina nthawi ya chipembedzo kumene ndi zinthu zimene anthu amakonda kuwiringula.

Tikufuna tione zinthu zimenezi mosabisa chifukwa choti sizidzakhala zinthu zophweka kusonkhanitsa anthu pamodzi tsiku la chipembedzo, komanso palibe mpingo umene umachita bwino pa nkhani imeneyi. Tonse ndife anthu ochimwa mu dziko limene lasokonezedwa ndi tembelero la uchimo, ndi chifukwa chake nkhani ya chipembedzo singalephele kukhala ngati phili la nkhondo nthawi zina. Tiyitenge kuti imeneyi ndi nkhondo ya uzimu.

Mpingo wopanda mavuto ndi okhawo umene uli kumwamba.

Ndi chifukwa chake nkoyenelera kuti tiphuzile kuti kodi chipembedzo ndi chani, komanso tionetsetse kuti sitikulolera tchimo lathu kapena zolakalaka zathu zitisokoneze pa nkhani ya chipembedzo. Ndi chifukwa chake lero tikufuna tiyankhe funso limeneli la kuti kodi tipembedze motani ndi mpingo wathu?