Pali zifukwa zambiri zimene zimapangitsa kuwerenga Baibulo kukhala chinthu chovuta, koma chifukwa chodziwikilatu – komanso chokhazikika – chimene chimapangitsa kuwerenga Baibulo kukhala chinthu chovuta ndi tchimo. Tikuyenela kuvomeleza kuti uchimo umatisokoneza.
Ø Aefeso 2:1-3 akunena kuti: “Ndipo inu adakupatsani moyo, pokhala mudali akufa ndi zolakwa ndi zochimwa zanu; Zimene mudayendamo kale, monga mwa mayendedwe adziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wamlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana akusamvera. Amene ife tonsenso tidagonera pakati pawo kale, mzilakolako za thupi lathu, ndi kuchita chifuniro cha thupi, ndi za maganizo, ndipo tidali ana a mkwiyo chibadwire, monganso wotsalawo.”
Ø Ndime imeneyi ikutiphuzitsa kunena kuti: anthu osakhulupilira ali akufa mu zolakwa zawo komanso machimo awo.
Ø Ndipo ngati tili amoyo mwa Khristu, idalipo nthawi imene ife tidali anthu akufawo.
Ø Mwa chikhalidwe chathu ndife ana a mkwiyo.
Ø Ndiye pamenepa tikuona kuti chinthu chimodzi chofunikila ndi chakuti: kuwerenga Baibulo kumatsutsana ndi chikhalidwe chathu cha uchimo. Ngakhale tili anthu okhulupilira ndipo mphamvu ya uchimo idagonjetsedwa mwa ife, chikhalidwe chathu cha uchimo chimakhala chikulimbanabe ndi kuwerenga Baibulo.
Ø Chiphuzitso chimene chimanena kuti munthu ukatembenuka mtima uchimo umachokelatu ndipo umayenda m’moyo osalimbana ndi tchimo nthawi zonse ndi chiphuzitso chabodza, sichichokela pa Mawu a Mulungu. Chimene Baibulo limatitsimikizila ndi chakuti: pamene munthu watembenuka mtima wayamba nkhondo yakulimbana ndi uchimo.
Ø Tikakamba pa nkhani yakuwerenga Baibulo, ndiye kuti pali mbali ina ya ife imene nthawi zonse imayesetsa kuti tisakhale ndi chizolowezi chakusanthula Malemba Opatulika. M’mawu ena titha kunena kuti, nthawi zonse zimene ife tinyamula Baibulo ndi kuyamba kuwerenga, tikumenya nkhondo – nkhondo pakati pa umunthu wathu wakale komanso komanso umunthu wathu watsopano. Akolose 3:1-17.