Kuwerenga Baibulo ndi kofunikila kwambiri. Tikaphuzitsa mtundu wa akhristu amene akudziwa kuphuzila, kukhala komanso kukonda Mau a Mulungu, tidzawakozekeletsa kukumana ndi china chilichose chobwela m’dziko.
Tikakamba za Baibulo tikutanthauza za mabuku 66 ogawidwa mu zipangano ziwiri. Chipangano chakale mabuku 39 komanso chatsopano mabuku 27.
Tikawelenga Baibulo timaphuzila zambiri za m’mene munthu alili komanso tanthauzo la moyo. Limatidziwitsa za Mulungu amene anatilenga komanso amene ali gwelo la dziko lonse. Mulungu amadzivumbulutsa yekha kwa ife kudzera m’Baibulo amene afunanso kuyanjana nafe.