LERO TIKUFUNA TIONE ZA UDINDO WA AZIMAYI MU MPINGO
Genesis 1:26-27; 2:19-25
1 Timothy 2:8-15
Chiphuzitso cha mpingo ndicho chimene tikulondola.
Mongokumbutsana tizindikile kunena kuti ulamuliro wathu pa china chilichonse chimene tifuna kuphuzila umachokela m’Baibulo. Ndi chifukwa chake pamene timayamba program imeneyi ya Chuma Mzikho Zadothi, tidayamba kuona kuti kodi Baibulo ndi chani. Cholinga chake chinali cha kuti tidzipatse poyambila kuti china chilichonse chokambidwa pa program imeneyi chichokele m’Mawu a Mulungu.
POYAMBA TIYENI TIONE MTSUTSO UMENE UMAKHALAPO PA NKHANI YA UDINDO WA AMAYI MU MPINGO.
Ayuda ena anali kuphuzitsa kunena kuti mkwabwino kutentha Mawu a Mulungu kusiyana ndi kuphuzitsa mzimayi. Ndineneletu kuti palibe munthu wowerenga Mawu a Mulungu ndi chidziwitso amene angakhulupilire fundo imeneyi. Chifukwa chiyani? Yesu anali kuphuzitsa azimayi mwaufulu komanso mokondwera ndipo anali kugwila nawo ntchito mnjira zosiyanasiyana.
VUTO LIMENE LILIPO LERO LINO PA MTSUTSO UMENEWU WA UDINDO WA AZIMAYI MU MPINGO NDI KUSOKONEKELA KWA ANTHU KOMANSO KUSOWEKELA CHITSIMIKIZO CHA MAWU A MULUNGU.
Anthu masiku ano angofika potsutsa china chilichonse chimene sakuchivetsa bwino m’Mawu a Mulungu. Chimene Mulungu adafotokozela m’Mawu ake pa dongosolo la udindo wa azimayi mu mpingo zangofika pooneka zopanda pake. Anthu asokonekela.
Kuonjezela pamenepo, mpingo nawo uli kakasi pa nkhani imeneyi. M’malo moyankha nkhani imeneyi ndi ulamuliro komanso mosakayika, mpingo wakhala ngati gulu la nkhondo losowa chochita. Mpingo wangofika pokana kukhala ngati nkhani imeneyi sikutikhudza.
Vuto linanso litha kukhala kuti mwina mpingo ulibe chidziwitso chokwanila kapena suli okonzeka kugwada pansi pa ulamuliro wa Baibulo. Anthu asokonekela.
Chimenechi chinayenela kuchitika ndi kuzindikila ulamuliro wathu kuti ukuchokela pa Baibulo kenako ndi kuyankhula mopanda mantha komanso moveka bwino. Kusokonekela kumene kulipo kwapezanaso ndi kusatsimikizika kwa mpingo pa chiphuzitso cha Mawu a Mulungu pa za udindo wa azimayi mu mpingo.
Tisalore dziko lapansi kuti lisinthe chikhulupiliro chathu pa Mawu a Mulungu. Ena akumanena kuti mpingo tikuyenela kumayenda ndi dziko chimene ndi chinthu chamanyazi. Mpingo sukuyenela kumayenda ndi dziko, tikuyenela tiziyenda monga mwa Mawu a Mulungu. Nkhani za gender zisasinthe chikhulupiliro chathu.
ZINTHU ZITATU ZOFUNIKILA NDIKAMBE PA NKHANI IMENEYI
Ndikudziwa kuti pali mabuku ambiri amene alembedwa osemphana ndi zimene Baibulo limakamba za udindo wa azimayi mu mpingo. Ndikudziwanso kuti nkhani imeneyi imatengedwa yopepuka ndi anthu ena. Ndipo zimenezi zitha kundipangitsa kuti nanenso ndingovomeleza zimene ena akuchita kutaya Mawu a Mulungu.
Koma ngakhale mabuku ambiri alembedwa otsutsana ndi chimene Baibulo limatiphuzitsa pa nkhani imeneyi, palibe umboni okwanila kuti anthu apeza katanthauzidwe kena katsopano kokhudzana ndi nkhani imeneyi kupatula kunena kuti chimene akuchita anthuwo ndi kunyozela Baibulo.
Nkhondo yaikulu sikukhudzana ndi kufanana kwa azibambo ndi azimayi. Nkhani yaikulu ndi ulamuliro wa Baibulo. Ndipo ngati titsimikizika mtima pamenepo tidzakhala ndi mphamvu, chikondi komanso chilimbikitso. Azitsogoleri ambiri lero lino ayesedwa kwakukulu pa nkhani ya ulamuliro wa Baibulo. Kodi timakhulupilira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu kapena muli Mawu a Mulungu? Iwo amene amakhulupilira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu sangatsutsane ndi chimene Baibulo likukamba pa nkhani imeneyi. Koma iwo amene amakhulupilila kuti mu Baibulo muli Mawu a Mulungu ndi amene akubweletsa chisokonezo mu mpingo wa Khristu.